African Storybook
Menu
Kambewu: Nkhani ya Wangari Maathai
Gridon Mwale
Maya Marshak
CiNyanja
Pamudzi  wina womangidwa pamatero ya phiri la Kenya kumwawa
kwa Africa,  Kunali kamtsikana kena
dzina lake Wangari. Wangari ndi amai ake anali kugwira ntchito zaminda.
Wangari
 anali mtsikana wokonda kucezera
pabwalo. Tisku lina Wangari anagaula mudimba mwao nabzyala tumbewu pansi
pomwe panali potentha kwambiri.
Thawi
imene anali kukonda kwambiri mtsikanayu tsiku lililonse inali pamene dzuwa
litangolowa kumene. Ndipo mudima ukagwira chakuti zomera zamthengo zaleka
kuoneka, Wangari anali kudziwa kuti thawi yopita ku nyumba yafika tsopano. Ndipo
popita kunyumba anali kudzera njira zang’ombe, kuwoloka mitsinje ndi kudutsa
minda mpaka kufika kwao.
Wangari
anali mwana wocenjera kwambiri ndipo anali wofunitsitsa kupita kusukulu
kukaphunzira. Koma makolo ake sanafune kuti kamtsikana aka kaphunzire koma kazikhala
pa nyumba ndi kugwira ncthito. Pamene Wangari anali ndi zaka 7, mukulu wake
wamwamuna anagonjetsa makolo awo pokambirana kuti Wangari apite kusukulu akaphunzire.
Wangaari
anakonda kuphunzira kwambir chotero kuti anaphunzira kopitirira kupyolera mkuwerenga
mabuku osiyanasiyana. Ndipo anakhoza kwambiri pa sukulu chotero kuti anapeza umwayi
wokaphunzira ku dziko lakutali la United States of America. Wangari
anasangalala kwambiri chifukwa anali kufunitsitsa kudziwa zambiri zapa dziko
lapansi.
Wangari
anaphunzira zinthu zambiri pamene anali pa American Univeziti. Anaphunzira pa
zomera ndi mumene zimakulira. Zimenezi zinamukumbutsa mumene anali kusewerera
ndi abale ake mthunzi ya mitengo mthengo laku-dziko lokongola la Kenya.  
Pamene
anali kuphunzira tsiku ndi tsiku anazindikira kuti akonda anthu akwao ku
Kenya. Anali kufuna kuti anthu kudziko limeneli tsiku lina akapate ufulu ndi mtendere.
Ndipo anayewa dziko lakwao pamene anapitiliza ndi maphunziro. ake kwakanthawi.
Anabwerera
kudziko lakwao ku Kenya pamane anamaliza maphunziro ake ndipo nthawi imeneyi dziko
la Kenya linali litasintha. Mapulazi akuluakulu anatenga malo ochuluka.
Azimai anali kusowa kotheba nkhuni chifukwa mitengo kunalibe. Anthu anali osauka
ndipo ana anali kuoneka anjala.
Wangari
anali kudziwa chofunika kuchita kuti athetsa mabvuto amenewa: anaphunzitsa
azimai kubzyala mitengo kuchokera kumbewu. Azimai amenewa anayamba kugulitsa
mitengo zao zitakula ndikupeza ndalama zosamalira ma banja awo. Chifukwa
cacimenechi azimai anakhala wokondwera kwambiri ndi Wangari amene anawa
thandiza kuti akhale ndi mphanvu komanso 
olimba.
Patapita
zaka zambiri, mitengo zimene zinabzyalidwa zija, zinakula ndi ku panga thengo.
Mitsinje inayambanso kukhala ndi madzi. Mbiri ya Wangari inafika ponseponse
mu Africa. Lerolino, mitengo zamitundumitundu mamilyoni tilikuonazi zinachokera
ku mbewu ya Wangari.
Wangari
anasewenzadi mwamphanvu. Chotero kuti anthu dziko lonse lapnansi anazindikila
ntchito yaikula yomwe anacita, ndipo ana patsidwa mphoto yodziwika kwambiri
padziko lonse lapansi. Mphoto imeneyi inali kutchedwa kuti Kulemekezedwa ndi
Mtendere, ndipo anakhala mkazi woyamba mu Africa kulandila mphoto yotero.
Wangari
anamwalira mu caka ca 2011, koma timamukumbukila tikamaona mtengo wokongola uliwonse
mthengo.
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kambewu: Nkhani ya Wangari Maathai
Author - Nicola Rijsdijk
Translation - Gridon Mwale
Illustration - Maya Marshak
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs
© Nicola Rijsdijk, Maya Marshak, Tarryn-Anne Anderson, Bookdash.org and African Storybook Initiative 2015
Creative Commons: Attribution 4.0
Source www.africanstorybook.org
Original source www.bookdash.org
Menu
  • Navigate

    Navigate through the story by swiping right or left or clicking when the cursors changes to an arrow on the right or the left edge of the screen.

    Tap or click on the centre of the page to see, or remove the menu bars at the top and the bottom of the screen. You can also use the ESC key.

    You can use the slider at the bottom as a way to move quickly through the story. On a mobile device tap on the slider before you drag the slider button.

    Click or tap to return to African Storybook.

  • Share
    If you have a Twitter or Facebook account, you can share this story on your page or a page you manage. You can also copy the web link (URL) for this story.
    • Twitter
    • Facebook
    • Url
  • Rate
    Other visitors rated this story

    Tell us how much you liked the story – drag the scroller to highlight one or more stars
    • Submit
  • Comment
    Read other people’s comments on the story, or add your own.
    • Enter your comment
    • Name
    • E-mail
    • Post
  • Translations and adaptations
    • 'n Klein Saadjie: Die Verhaal Van Wangari Maathai
      Afrikaans (Translation)
    • البذرة الصغيرة – حكاية ونقاري ماتهاي
      Arabic (Translation)
    • Abasem a ɛfa Wangari Maathai
      Asante Twi (Translation)
    • Njere yaing'ono: Nkhani ya Wangari Maathai
      ChiChewa (Translation)
    • A tiny seed: The story of Wangari Maathai
      English (Original)
    • Making new forests
      English (Adaptation)
    • A tiny seed (Colour-in)
      English (Adaptation)
    • Une Petite Graine: L'Histoire De Wangari Maathai
      French (Adaptation)
    • Une Petite Graine: L’Histoire De Wangari Maathai
      French (Translation)
    • Awdi Cewndi: Geccawol Wanderimam Danasabe
      Fulfulde (Translation)
    • Awre peetel: Taaria Wangari Maathai
      Fulfulde Adamawa (Translation)
    • Mitsitsin Iri: Labarin Wangari Maathai
      Hausa (Nigeria) (Translation)
    • Yayyan Biciyoyi: Labaru Wanderimam Danasabe
      Hausa (Nigeria) (Translation)
    • Ulubuto Lunoono: Inshimi ya kwa Wangari Maathai
      IciBemba (Translation)
    • Ukhozo lwembewu oluncinane
      isiXhosa (Translation)
    • Imbewu encane
      isiZulu (Translation)
    • Nɨng py∂nɨng a Nyang-Sh∂ng:
      Jenjo (Translation)
    • Akabuto gato: Inkuru ya Wangari Maathai
      Kinyarwanda (Translation)
    • Wangari Maathai
      Kiswahili (Adaptation)
    • Wangari Maathai
      Kiswahili (Adaptation)
    • Hadithi kumhusu Wangari Maathai
      Kiswahili (Translation)
    • Sin titinyang: Chisung na Wanderimam Danasabe
      Kuteb (Translation)
    • Shiŋgoòy: Kimfèr Ke Wangari Mathay
      Lámnsoʼ (Translation)
    • Mukasigo akato: Olugero lwa Wangari Maathai
      Luganda (Translation)
    • Ensigo Entono
      Lusoga (Translation)
    • Gel Tuh Teri: Mul Wanderimam Danasabe
      Mambilla (Nigeria) (Translation)
    • Nderhere Nsungunu
      Mashi (Translation)
    • Jĩng Vu seseere: Ruu ka yuu Waawi Maading
      Mumuye (Translation)
    • Aŋerio ôllô odiha ꞌtô: Wangari Maathai
      Otuho (Translation)
    • Uma sementinha: A História de Wangari Maathai
      Portugues (Translation)
    • Peu ye nnyanennyane
      Sepedi (Translation)
    • Peo e nyane
      Sesotho (South Africa) (Translation)
    • Embicha Tsubuh: Esuh Wangari Maathai
      Tigun (Translation)
    • Ishange Kon I Kiriki
      Tiv (Translation)
    • Èso Kékeré Kan: Ìtàn Tí Wangari Maathai
      Yoruba (Adaptation)
  • Download to read
    Landscape version
  • Download to print
    Portrait (booklet) version
  • Download EPUB