Kuwerenga nyama
Ausward Siwinda and Peter Msaka
Rob Owen


Njovu imodzi ikupita kokamwa madzi.
Akadyamnsonga awiri akupita kokamwa madzi.
Njati zitatu ndi mbalame zinayi zikupitanso kokamwa madzi.
Agwape asanu ndi akaphulika asanu ndi mmodzi zikupita kokamwa madzi.
Mbidzi zisanu
ndi ziwiri zikuthamangira kokamwa madzi.
Achule asanu ndi atatu ndi nsomba zisanu ndi zinayi zikusambira m'madzi.
Mkango umodzi ukubangula. Ukufunanso kumwa madzi.
Ndani akuopa Mkango?
Njovu imodzi ikumwa madzi ndi Mkango.
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kuwerenga nyama
Author - Clare Verbeek, Thembani Dladla and Zanele Buthelezi
Translation - Ausward Siwinda and Peter Msaka
Illustration - Rob Owen
Language - Chichewa
Level - First words
© School of Education and Development (UKZN) and African Storybook Initiative 2007
Creative Commons: Attribution 4.0
Source www.africanstorybook.org
Original source http://cae.ukzn.ac.za/resources/seedbooks.aspx


