Chibasi chabuluu
Mecelin Kakoro
Mango Tree

M'mudzi wa Limbani mumadutsa basi imodzi yokha. Inali yayikulu ya mtundu wa buluu.

Inali ya phokoso kwambiri.

1

"Mawa tipita ku tawuni," anatero amayi a Limbani.

"Tikagula yunifolomu yako."

2

Limbani anasangalala kwambiri. Adzakwera basi yayikulu yabuluu.

Usiku umenewo Limbani sanagone.

3

Amayi ake atabwera kudzamudzutsa, Limbani anali atavala kale.

4

Limbani ndi amayi ake anayenda kupita kokwerera basi. Anayidikira basi yayikulu yabuluu ija.

Koma basi siinafike.

5

Anthu ena anafika pokwerera basi. Anadandaula chifukwa basi inachedwa.

"Basi ifika nthawi yanji?" anafunsa motero.

6

Limbani anadandaula. "Sitipita ku tawuni," anaganiza choncho.

"Sindikhala ndi yunifolomu yatsopano."

7

Anthu ena anatopa kudikira ndikubwerera kunyumba kwawo.

Limbani analira. Samafuna kubwerera kunyumba. "Tidikirabe," anatero mayi ake.

8

Mwadzidzidzi, anamva phokoso. Anawona fumbi m'mwamba.

Basi ija imabwera!

9

Koma siinali basi yabuluu. Siinalinso basi yayikulu. Inali basi yofiira komanso yaying'ono.

Anthu sanafune kukwera basi imeneyi.

10

"Kwerani! Kwerani! Tachedwa kwambiri lero," anakuwa woyendetsa basi.

11

Limbani ndi mayi ake anali oyamba kukwera.

Kenako ena onse anakwera basi yofiira yaying'ono ija.

12

Limbani anawona kunja kudzera pa zenera.

Anawona anthu ambiri pokwerera basi paja.

13

Anthu ena ambirinso anathamangira basi ija. Koma anachedwa kwambiri.

Basi yofiira ija inali itadzadza. Inanyamuka kupita ku tawuni.

14

"Basi yabuluu yaikulu ija ili kuti?" anafunsa amayi a Limbani.

"Yawonongeka. Tikuikonza. Ibwera mawa," anayankha woyendetsa basi uja.

15

Limbani sanasamale za mtundu wa basi. Sanasamale za kukula kwa basi.

Basiyi imapita ku tawuni!

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Chibasi chabuluu
Author - Mecelin Kakoro
Translation - Peter Msaka
Illustration - Mango Tree
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs