Munthu wamtali kwambiri
Cornelius Wambi Gulere
Catherine Groenewald

Khasu lake linali lalifupi kwambiri.

1

Khomo la nyumba yake linali lalifupi kwambiri.

2

Bedi lake linali lalifupi kwambiri.

3

Njinga yake inali yayifupi kwambiri.

4

Munthuyu anali wamtali kwambiri.

5

Anapanga mpini wa khasu wautali kwambiri.

6

Anapanga khomo lalitali kwambiri.

7

Anapanganso bedi lalitali kwambiri.

8

Anagula njinga yaitali kwambiri.

9

Anakhala pa mpando wautali kwambiri.

Amadyera foloko yaitali kwambiri.

10

Anasamuka m'nyumba yake ndikukakhala ku nkhalango. Anakhalako zaka zambiri.

11
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Munthu wamtali kwambiri
Author - Cornelius Wambi Gulere
Translation - Peter Msaka
Illustration - Catherine Groenewald
Language - ChiChewa
Level - First words