Awa ndi aphunzitsi anga. Ndipo dzina lawo ndi a Akinyi.
Iwo amatikonda kwambiri.
Aphunzitsi awa amatiphunzitsa kuwerenga.
Amatiphunzitsa zilembo za mavawelo. Ndingawerenge zilembo a. e, i, o, u.
Aphunzitsi Akinyi amatiphunzitsa za utoto monga kufiira, kubiriwira, msipu, cikasu ndi kuda.
Pa nthawi yogona, Aphunzitsi Akinyi amatiimbira nyimbo yogonera.
Nyimbo yogonera imaimbidwa tere:
Lulu wee, Lulu wee,
Mwana akalira ndi njala,
Mwana akalira ndi tulo,
Mwana akalira ndi njala,
Mwana akalira ndi tulo.
Aphunzitsi Akinyi amadziwa kunena nthano zambiri.
Tsiku lililonse la mlungu, iwo amatiuza nthano zosiyanasiyana.
Patsiku Lolemba, amatiuza nthano za amuna amene anacita zinthu zazikulu.
Patsiku Laciwiri, amatiuza nthano za azimayi amene anacita zinthu zaikulu.
Patsiku Lacitatu, amatiuza nthano zonena za mayendedwe.
Patsiku Lacinayi, amatiuza nthano zaulimi.
Ndipo patsiku Lacisanu, timakamba nthano zathu patokha.
Aphunzitsi athu ndi abwino koposa m'dziko lonse.
Ndikakula, ndifuna kuti ndikakhale ngati Aphunzitsi a Akinyi.