Maguru apasa miyendo
Mutugi Kamundi
Wiehan de Jager

Kalekale, nyama zonse zinalibe miyendo.

Izo zinali kukwawa pansi.

1

Ndi anthu cabe amene anali ndi miyendo imene Maguru anawapatsa.

2

Tsiku lina, Maguru anaganizira zopatsa nyama zonse miyendo.

Iye amafuna kuti nyama ziziyenda.

3

Nyama zinakondwera kwambiri pamene zinamvera kuti zidzalandira miyendo.

Zinayimba ndi kuvina.

4

Nyama iliyonse inafuna kukhala ndi miyendo kuti iziyendera ndi kuthamangira.

Nyama zinanena kuti kukwawa kunali kovuta. Zinali kumva kuwawa.

5

Pamene Maguru anabwera, nyama zambiri zinapita kunyumba kwake.

Nyamalikiti, Mkango, Njovu, Akalulu, Ng'ona ndi Mbalame zinapanga mzere, kuti zipatsidwe miyendo.

6

Nyama iliyonse inapatsidwa miyendo inai.

Mbalame zinapatsidwa miyendo iwiri.

7

Zinthu zonse zinasintha pambuyo polandira miyendo.

Nyama zina zinavina ndicisangalalo. Nyama zina zinalephera kuyenda, ndipo zinagwa pansi.

8

Nyama zina zinzungulira m'mudzi kuonetsa anthu miyendo yawo.

Zonse zinati, "Sitidzakwawanso."

9

Nyama imene inali yomalizira mu mndandanda inali Bongololo. Maguru anafunsa Bongololo, "Pali ena omwe akukulondola pambuyo pako?"

"Iyayi kulibe, ndine womalizira," anayankha tero Bongololo.

10

Maguru anaganiza nati, "Ngati kulibe ena, kodi miyendo imene yatsala tidzacita nayo ciyani?"

Maguru anapatsa Bongololo miyendo yonse imene inatsalako.

11

Bongololo anayenda wokondwera kwambiri cifukwa anatenga miyendo yambiri.

"Ndidzayamba kuyenda mofulumira kuposa wina aliyense," anaganiza tero.

12

Pambuyo pakuti Bongololo wapita, Njoka inafika kunyumba kwa Maguru.

"Ndipatsenkoni miyendo nanenso," inapempha Njoka.

13

Maguru anati, "Ndapatsa kale miyendo. Nanga iweyo unali kuti?"

"Ndinagonerera," inayankha Njoka.

14

Maguru anafunafuna m'nyumb yake kuti kapena munatsalako miyendo iliyonse.

Sanapeze miyendo iliyonse.

15

Maguru anacoka panja nauza Njoka, "Cangoipa Njoka koma kulibe mendo yasalako." Njoka inakalaba, ndipo inabwerera kunyumba cilibe miyendo.

Kucokela ija siku, Njoka simagonelela. Masiku onse iyembekezela siku imene izakatenga miyendo.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Maguru apasa miyendo
Author - Mutugi Kamundi
Adaptation - Bether Mwale-Moyo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs