Mmene Nyerere inapulumutsira Nkhunda
Kholeka Mabeta
Wiehan de Jager

Linali tsiku lotentha mnkhalango youma.

1

Nyerere yaing'ono inalibe kwa masiku ambiri.

2

"Ndifuna madzi ocepa cabe, ngakhale dontho locokera kutsamba lamtengo," inatero Nyerere.

3

Koma ngakhale mame anali atauma.

4

"Ngati sindizamwa madzi, ndizafa ndi ludzu," kanadandula Kanyerere.

"Ndiyenera kuti ndipite kumtsinje umene ndamvera za mbiri yake."

5

"Mtsinje ndiwodzala ndipo uli ndi mphamvu, ndipo udzakuguza," anamucenjeza gologolo wanzeru.

6

Koma Kanyerere kanali ludzu kwambiri. "Ndidzafa ngati sindikumwa madzi."

Conco, Kanyerere kaja kanapita kukafuna mtsinje.

7

8

Kanapita pa udzu ndi nthambi zamtengo wouma kawmbiri.

9

Kanayenda mpaka kanamvera phokoso lamadzi. Unali mtsinje!

Kanamvera mafunde a madzi.

10

Kanyerere kanamwa madzi ozizira.

11

Kanakondwera kwambiri ndipo sikanamvere mafunde pamene anali kubwera.

12

Kanyerere kanayesa kugwila mauza yamene yanali kuyangalala pafupi pake.

Koma manzi yanakakanka ndipo kanadonsewa na manzi.

13

"Ndithandizeni! Ndithandizeni!" Kanaitana."

14

"Mofulumira, kwera apa," inatero Nkhunda yoyera, itagwiririra kamutengo mkamwa mwake.

15

16

"Nizankala pano kuti nionge zikomo kwa Nkunda," Kanyerere kanaganza.

"Nizayembekeza mpaka abwere kumwa manzi Nkhunda." Koma Nkhunda sanaonekele.

17

Tsiku lina pamene Kanyerere kanali kuyembekezera Nkhunda, anyamata awiri anabwera kumtsinje.

Anyamata awa anali ndi malegeni ophera mbalame.

18

"Pali Nkhunda yaikulu yoyera imene imabwera kuno kudzamwa madzi," anatero mnyamata m'mmodzi.

"Lero usiku tidzayidya."

19

20

"Sindidzalekerera anyamata awa kuti aphe Nkhunda yoyera," kanaganiza tero Kanyerere.

"Ndine wamng'ono kwambiri, koma ndingacite ciyani?"

21

Pamenepo, Nkhunda yoyera inauluka kutsikira pansi kuti imwe madzi.

22

23

Kanyerere kaja kanaganizira zocita.

24

Kanalumphira pamwendo wa mnyamata m'modzi.

Kanyerere kanaluma mnyamata uja ndi mphamvu zake zonse.

25

Mnyamata analuumpha.

Ndipo anakuwa nati, "Mayo! Mayo!"

26

Nkhunda yoyera inadabwa ndipo inauluka ndi kupulumukira kucitetezo.

27

Ndiponso ndiye mwamene Kanyerere kana ongela Nkhunda yotuba cifukwa co pulumusa umoyo wake.

28
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mmene Nyerere inapulumutsira Nkhunda
Author - Kholeka Mabeta, Judith Baker
Adaptation - Bether Mwale-Moyo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - First sentences