Kufunsa Funsa kwa Kamwana ka Njovu
Judith Baker
Wiehan de Jager

Antu onse aziba kuti ili na mpuno itali kwambili.

1

Koma kale kale mpuno ya Njovu inali ifupi ndipo yoyina.

Monga nsapato pakati pa cinso cake.

2

Siku lina, kamwana ka Njovu kanabadwa. Kanali kufunsa funsa pali aintu zonse.

Kanali kufusa cinyama ciliconse.

3

Kanali na mafunso kwa Nyamalikiti.

"Cifukwa ninji uli na mukosi utali?" Kanafunsa.

4

Kanali na mafunso kwa Cipembele.

"Cifukwa ninji nyanga yako niyakutwa?"

5

Kanali na mafunso kwa Mvuu.

"Cifukwa ninji uli na menso yofuwila?" kanafunsa.

6

Kanali na mafunso kwambili kwa Ng'wena.

"Kodi Ng'wena imadya cani usiku?" kalnafunsa.

7

"Osafunsa funsa mafunso yotelo!" anakamba amai ake.

Kamwana ka Njovu kanakalipa kananyamuka noyenda.

8

Mwamusanga musanga, mbalame ya Cikwangala inumbuluka nafika kuli kamwana ka Njovu.

Nanena nati, "Tiye nikonke kumusinje, komwe uzaona comwe Ng'wena ikudya usiku."

9

Sono Kamwana ka Njovu kanakonka Cikwangala kumusinje.

10

Kanapita mumauzu na imilila pambali pamusinje.

Kanalangana mumusinje. Ilikuti Ng'wena?

11

"Bwanji," Unakamba mwala pambali pamusinje.

"Bwanji," kanakamba ka Mwana ka Njovu. "Niuze comwe Ng'wena ikudya usiku?" kanafunsa.

12

"Fendela pansi nizakuuza," unakamba mwala.

"Fendela pafupi, pafupi," unakamba mwala.

Kamwana ka Njovu kanafendela pansi na pansi.

13

"Gwi!" mpuno ya Kamwana ka Njovu inagwidwa mu kamwa ka Ng'wena.

"Ng'wena izadya iwe usku," cinanena Cikwangala nambuluka.

14

Kamwana ka Njovu kanankala nazidosa na mendo yake ya mphamvu. Kanadonsa nodonsa.

Koma Ng'wena sinalekelele mpuno ya kamwana ka Njovu.

15

Mpuno ya Kamwana ka Njovu inadonseka, nadonseka, nadonseka.

"Dii!" Kanazigwera pamusana Kamwana ka Njovu.

16

Ng'wena ina mbila mu manzi.

Inakalipa cifukwa cotaya cakudya cake ca usiku.

17

Kamwana ka Njovu kanalangana mpuno yake. Inadonseka mpuno natalipa kwambili.

Kanakagiwa ku ona pamene inali kupela mpuno!

18

Ina talipa kwambili mpuno, ndipo Kamwana ka Njovu kanali kukwanisa ku tyola vipaso mumitengo mumwamba.

19

Mpuno yake ina talipa ndipo kanakwanisa kuzisambika pa musana na manzi.

Kucokela apo, zonse njovu zili na mpuno zitali.

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kufunsa Funsa kwa Kamwana ka Njovu
Author - Judith Baker, Lorato Trok
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs