Nkuku ndi Bongololo
Winny Asara
Magriet Brink

Nkhuku ndi Bongololo anali abwenzi. Anali abwenzi opikisana wina ndi mnzake.

Tsiku lina, iwo anaganiza zocita masewero a mpira, kuti aone ymwe angakhale wopambana.

1

Iwo anapita kukasewera mpira wa miyendo ndipo anayamba masewero awo.

Nkhuku inali yofulumira, koma Bongololo anali wofulumira koposa. Nkhuku inamenyera mpira kutali, koma Bongololo anaposa pamenepo.

Nkhuku inakalipa.

2

Iwo anaganizira zomenya mpira wa mapenauti. Bongololo anali woyamba kukhala m'golo, ndipo Nkhuku inagoletsa cigoli cimodzi cabe.

Pambuyo pake iwo anasinthana, Nkhuku inakhala pa golo.

3

Bongololo anamenya ndipo anagoletsa. Bongololo anacita njomba ndipo anagoletsa. Bongololo anagunda mpira ndi mutu, ndipo anagoletsa.

Bongololo anagoletsa zigoli zisanu.

4

Nkhuku inakalipa kuti inaluza. Inakalipa cifukwa inaluza moipa.

Bongololo anayamba kuseka cifukwa mnzake anayamba kulongolola.

5

Nkhuku inakalipa kwambiri kwakuti potsirizira pake inameza Bongololo.

6

Pamene Nkhuku inali kupita kupita kunyumba, anakumana ndi amai ake Bongololo. Amake Bongololo anafunsa nati, "Kodi mwamuonako mwana wanga?"

Koma Nkhuku siyinawayankhe Amake Bongololo. Amake Bongololo anada nkhawa.

7

Pambuyo pake, Amake Bongololo anamva liu lotsika, "Ndithandizeni amai!" linadandaula liulo.

Amake anapenya mowazungulira ndi kumvetsera mosamala. Liulo linacokera m'mimba mwa Nkhuku.

8

Amake Bongololo anakweza mau nati, "Gwiritsa nchito mphmvu zako zapadera mwana wanga!"

Abongololo angapange fungo loipa ndi kumveka moipa mkamwa. Nkhukuinamva kudwala kwambiri.

9

Nkhuku inageya. Pambuyo pake inameza mata ndi kulavula. Pambuyo pakenso, inayetsemula ndi kukhosomola. Ndi kukhosomola.

Bongololo anamveka kuipa mkamwa.

10

Nkhuku inakhosomola kufikira anakhosomola Bongololo.

Amake Bongololo ndi mwana wawo anakwawira kumtengo ndi kubisala.

11

Kucokela apo, pakati pa Nkuku ndi Bongololo pali cizondo.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nkuku ndi Bongololo
Author - Winny Asara
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Magriet Brink
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs