Basi yaikulu yobiriwira
Mecelin Kakoro
Mango Tree

Munali cabe basi imodzi cabe m'mudzi wa Mangani. Basiyo inali yaikulu ndi yobirwira.

Ianali basi yaphokoso kwambiri.

1

"Mawa tidzapita kutauni," anatero amai ake Mangani. "Tidzagula yunifomu yako mawa."

2

Mangani anasangalala kwambiri. Iwo akanapita paulendo mu basi yaikulu yobiriwira.

Usiku umenewo, Mangani sanagone.

3

Pamene amai ake anabwera kudzamudzutsa, Mangani anali atadzuka kale ndipo anali atavala zovala zake.

4

Mangani ndi amai ake anayenda ndi miyendo kukafika ku citesheni ca basi.

Iwo anayembekezera basi yaikulu yobiriwira. Koma basi ija siinabwere.

5

Anthu ena anafika pa citesheni ca basi. Iwo anadandaula cifukwa cakuti basi inacedwa kufika.

"Kodi basi ilikuti?" iwo anafunsa.

6

Mangani anadandaula. "Sitidzapita kutauni," iye anaganiza.

"Sindidzakwanitsa kugula yunifomu yanga."

7

Anthu ena analema kuyembekezera ndipo anapita kunyumba. Mangani anadandaula. Sanafune kuti abwerere kunyumba.

Amai ake anati, "Tidzayembkezako panng'ono."

8

Mwadzidzidzi, iwo anamva phokoso. Iwo anaona fumbi m'mwamba.

Basi inali kubwera!

9

Koma basi siinali yobiriwira. Siinalinso yaikulu. Basiyo inali yofiira ndipo yaing'ono.

Anthu sanafune kukwera m'basi imeneyi.

10

"Lowani! Lowani!" anatero dalaivala. "Tacedwa kwambiri lero," anatero iye.

11

Mangani ndi amai ake anambirira kulowa m'basimo.

Pambuyo pake wina aliyense analowa mu basi yofiira imeneyi.

12

Mangani anapenya pawindo.

Iye anaona anthu ambiri pa citesheni.

13

Anthu ena ambiri anathamanga kuti akwere basi ija. Koma iwo anacedwa kwambiri.

Basi yofiira inali itadzala ndi anthu. Iyo inanyamuka ulendo wopita kutauni.

14

"Kodi basi yaikulu?" anafunsa amai ake Managi.

"Basi ija yafa," anayankha tero adalaivala. "Tikuikonza lero. Idzabwera mawa."

15

Mangani sanavutike na kaonekedwa ka basi. Sanavutike na kucepa kapena kukula kwa basi.

Anakondwela cifukwa iyi basi inali kuyenda ku tauni!

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Basi yaikulu yobiriwira
Author - Mecelin Kakoro
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Mango Tree
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs