Zama ndi wopambana!
Michael Oguttu
Vusi Malindi

Mchimwene wanga wamng'ono amagona mochedwa.

Ndimadzuka mofulumira chifukwa ndine wopambana.

1

Ndine amene ndimalowetsa kuwala kwa dzuwa m'nyumba.

2

"Ndiwe nthanda yanga," amayi anena.

3

Ndimasamba tsiku ndi tsiku, sindifuna kuthandizidwa.

4

Sindidandaula kusamba madzi ozizira kapena kusambira sopo wochapira zovala.

5

Amayi andikumbutsa, "Usayiwale kutsuka mano."

Ndiyankha, "Sizingatheke kuiwala."

6

Ndikamaliza kusamba, ndimapereka moni kwa agogo amuna ndi azakhali.

Ndimawafunira mafuno abwino atsikulo.

7

Kenako ndimavala zovala.

"Tsopano ndine wamkulu, amayi," nditero.

8

Ndimatha kumanga mabatani ndi nsapato.

9

Ndimayesetsa kudziwitsa m'chimwene wanga nkhani za kusukulu.

10

M'kalasi ndimalimbikira kwambiri.

11

Ndimachita zabwino zonsezi tsiku ndi tsiku.

Koma chomwe ndimakonda kwambiri ndi kumangosewera!

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Zama ndi wopambana!
Author - Michael Oguttu
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Vusi Malindi
Language - Chichewa
Level - First sentences