"Amayi," ayitana Lebo.
"Tabwerani muone. Zovalazi zikundithina!" Mayi amuyankha, "Ndione."
"Tawonani siketi yanga. Ndi yaying'ono kwambiri," atero Lebo.
"Eya, ndi yaying'ono," atero mayi "Nomsa atha kutenga ikhale yake."
"Tawonani jinzi yanga. Ndi yaying'ono kwambiri," atero Lebo.
"Eya, ndi yaying'ono." Atero mayi. "Nomsa atha kutenga ikhale yake."
"Tawonani tisheti yanga. Ndi yayin'gono kwambiri," Atero Lebo.
"Eya, ndi yaying'ono." Mayi atero. "Nomsa atha kutenga ikhale yake."
"Tawonani juzi yanga. Ndi yaying'ono kwambiri," atero Lebo.
"Eya, ndi yaying'ono," mayi atero. "Nomsa atha kutenga ikhale yake."
"Tawonani lenikhoti yanga. Ndi yaying'ono kwambiri," atero Lebo.
"Eya, ndi yaying'ono," atero mayi. "Nomsa atha kutenga ikhale yake."
Tawonani masokosi anga. Ndi ang'ono kwambiri." Atero Lebo.
"Eya, ndi ang'ono." Atero mayi. "Nomsa atha kutenga akhale ake."
"Tawonani nsapato zanga. Ndi zazing'ono kwambiri." Atero Lebo.
"Eya, ndi zazing'ono." Atero mayi. "Nomsa atha kutenga zikhale zake."
"Tsopano uli ndi zovala zambiri," atero Lebo.
"Oooo! ayi," atero Nomsa. "Zovalazi ndi zazikulu kwambiri kwa ine!"