Aphunzitsi a Akinyi
Lawrence A. Konjuro
Vusi Malindi

Awa ndi aphunzitsi anga.

Dzina lawo ndi a Akinyi.

Amatikonda kwambiri.

1

Aphunzitsi a Akinyi amatiphunzitsa mndandanda wa zilembo.

Amatiphunzitsa zilembo za liwu.

Nditha kutchula zilembo izi a, e, i, o, u.

2

Aphunzitsi a Akinyi amatiphunzitsa mitundu.

Ndimadziwa mtundu wofiira, wabuluu, wagirini, wayelo, ndi wakuda.

3

Nthawi yopumula timagona, aphunzitsi a Akinyi amatiimbira nyimbo kuti tigone.

Amatiimbira kanyimbo kogonetsera ana.

4

Nyimboyo imati:

Goonaa mwaanaa, goonaa mwaanaa.
Uleke kuliraa, uleke kuliraa.

Mbalame zonse zagona mu zisa zawo zazing'ono. Goonaa mwaanaa, goona mwaanaa.

5

Aphunzitsi a Akinyi amadziwa nyimbo zambiri.

Amatikambira nkhani yatsopano tsiku lililonse.

6

Lolemba, amatikambira nkhani zokhudza abambo amene anachita zazikulu.

7

Lachiwiri, amatikambira nkhani zokhudza amayi amene anachita zazikulu.

8

Lachitatu, amatikambira nkhani zokhudza mtengatenga ndi mtokoma.

9

Lachinayi, amatikambira nkhani za ulimi.

10

Lachisanu, timanena nkhani zathu.

11

Aphunzitsi athu ndi opambana ena onse pa dziko.

Ndikadzakula, ndifuna kudzakhala ngati aphunzitsi a Akinyi.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Aphunzitsi a Akinyi
Author - Lawrence A. Konjuro
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Vusi Malindi
Language - Chichewa
Level - First sentences