Chilango
Adelheid Marie Bwire
Melany Pietersen

Tsiku lina, amayi anagula zipatso zosiyanasiyana.

1

"Kodi zipatsozi tidya nthawi yanji?" Tonse tinafunsa.

"Tidya zipatso zimenezi usiku uno," anatero amayi.

2

Mchimwene wanga Rahim ndi wadyera.

Analawa zipatso zonse. Ndipo anadya zambiri.

3

Taonani zimene wachita Rahim!" anakuwa mchimwene wanga wamng'ono.

"Rahim ali ndi khalidwe loipa komanso lodzikonda," ndinanena.

4

Amayi anakwiya ndi Rahim.

5

Tonse tinakwiya ndi Rahim.

Koma Rahim sanafune kupepesa.

6

"Kodi mumulanga Rahim?" anafunsa mchimwene wanga wamng'ono.

7

"Rahim, upepesa posachedwapa," anamuchenjeza amayi.

8

Rahim anayamba kusamva bwino.

9

"Mmimba mwanga mukuwawa," Rahim ananong'ona.

10

Amayi anadziwa chifukwa chiyani Rahim anayamba kudwala.

"Zipatso wadya zija zikumulanga ameneyo." Amayi anaganiza choncho.

11

Pamapeto pake, Rahim anatipepesa tonse.

"Sindidzachitanso dyera," analonjeza motero.

Tonse tinakhulupilira zimene ananenazo.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Chilango
Author - Adelheid Marie Bwire
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Melany Pietersen
Language - Chichewa
Level - First sentences