Maguru apereka miyendo
Mutugi Kamundi
Wiehan de Jager

Kalekale, nyama zonse zinalibe miyendo.

Zinkayenda chokwawa.

1

Anthu okha ndi amene anali ndi miyendo, yomwe Maguru anapereka.

2

Tsiku lina, Maguru anaganiza zopereka miyendo kwa nyama iliyonse. Amafuna kuti nazo ziziyenda.

Anazifotokozera za ganizoli.

3

Nyama zinati, "Zikhala bwino kwambiri kukhala ndi miyendo."

Nyamazo zinayimba ndi kuvina.

4

Nyama zinanena kuti kukwawa kunali kovuta.

Zimamva kuwawa.

5

Tsiku litafika, nyama zambiri zinapita ku nyumba ya Maguru.

Akadyamnsonga, mikango, njovu, akalulu, ng'ona ndi mbalame zinayima pa mzere.

6

Nyama iliyonse inapatsidwa miyendo inayi.

Mbalame iliyonse inapatsidwa miyendo iwiri.

7

Zinthu zinasinthiratu nyama zitalandira miyendo.

Zina zinavina ndi chisangalalo. Zina zinagwa pansi.

8

Zinapita kukawonetsa anthu.

Nyama zinati, "Sitidzakwawanso."

9

Bongololo anali womaliza pa mzere. Maguru anafunsa, "Pali wina aliyense pa mbuyo pa iwe?"

Bongololo anayankha, "Ayi, Ndine womaliza."

10

Maguru anaganiza, "Uyu ndi womaliza. Nditani ndi miyendo yotsalayi?"

Maguru anapereka miyendo yonse yotsala kwa Bongololo.

11

Bongololo anasangalala kwambiri. Anati, "Ndiziyenda mofulumira kuposa ena onse."

12

Bongololo atachoka, Njoka inafika ku nyumba ya Maguru.

Ndipo inati kwa Maguru, "Chonde patseni miyendo."

13

Maguru anati, "Ndapereka miyendo yonse. Unali kuti?"

Njoka inayankha, "Ndinagonereza."

14

Maguru anafufuza ngati panali miyendo yotsala.

Sanapeze mwendo ngakhale umodzi.

15

Maguru anati kwa Njoka, "Pepa. Palibe miyendo yotsala." Njoka inakwawira ku nyumba opanda miyendo.

Kuyambira nthawi imeneyo, Njoka simagona tulo kwambiri. Ikudikira kuti idzakhale yoyamba kulandira miyendo.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Maguru apereka miyendo
Author - Mutugi Kamundi
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Wiehan de Jager
Language - Chichewa
Level - First paragraphs