Kumvetsera thupi langa
Noni
Angie and Upesh

Lero sindipita ku sukulu.

Ndi tsiku la tchuthi!

1

Lero sindiwonera kanema.

Kulibe magetsi.

2

Ndiye ndizitani?

Lero ndi mvetsera thupi langa!

3

Choyamba, ndikhale chete.

Kuti ndimvetsere thupi langa.

4

Eyaa, tsopano ndikutha kumvera kupuma kwanga.

Ndikupumira mkati ndi kunja, mkati ndi kunja.

5

Ndingathe kupuma mwaphokoso. Fweeee!

Komanso motsitsa. Shiiiiii!

6

Tsopano ndikumva kugunda kwa mtima wanga!

Gugu! Gugu! Gugu!

7

Kodi ndingauchititse mtima wanga kugunda mofulumira kapena mokweza?

Eya, pojowa kwa maulendo makumi awiri.

8

Tsopano onani, mtima wanga ukugunda mofulumira koposa.

9

Ndikayika zala zanga pothera mkono wanga, ndikumva kugunda kwa mtima.

10

Ndikudzimva ndikamaseka.

Hahahaa hahahaa, hahahaa!

11

Ndikudzimva ndikamalira.

Mayooo, Mayooo!

12

Ndikudzimva ndikamaomba m'manja.

Phwaaa, phwaaa, phwaaa.

13

Ndikumva mmimba mwanga mukamalira.

Gugululu, gugululu, gugululu.

14

Mimba yanga ikunena kuti, "Ndidyetse!"

15

Mphuno yanga ikununkhiza kuphikidwa kwa makeke m'khitchini la amayi anga.

Tsopano ndikufuna ndimve zibwano zanga zikutafuna makekewo.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kumvetsera thupi langa
Author - Noni
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Angie and Upesh
Language - Chichewa
Level - First sentences