Msungi ndi nyama za masiye
Nina Orange
Magriet Brink

Iyi ndi nkhani ya Msungi ndi malo ake osungirako ana a nyama za masiye.

1

Mwezi wa Ogasiti unali mwezi wotanganikitsa kwa Msungi ndi othandizira ntchito pa malopa.

2

Mkite anali woyamba kufika. Mkite anali ndi chaka chimodzi pamene anafika.

Anabwera pa chigalimoto chakale cha mtundu wa girini.

3

Msungi ndi omuthandiza ake anamumvera chifundo Mkite.

Anali woonda kwambiri komanso wosasangalala.

4

Koma posakhalitsa, Mkite anapeza mphamvu. Anayamba kusewera ndi nyama zinzake pa malopo.

5

Tsiku lina mwezi wa Ogasiti, ndege ya helikoputa inatera pa malowa.

6

Msungi ndi omuthandizira anathamangira panja.

Mu helikoputa munali kamwana ka njovu komwe kanafunditsidwa gombeza.

7

Dzina lake anali Ndiwa.

Anali khanda la masiku asanu. Msungi anadyetsa Ndiwa ndi botolo.

8

Wamasiye wachitatu kufika mwezi umenewo anali Malea.

Anafika pa therekitala yofiira. Anali wa miyezi isanu ndi umodzi.

9

Malea anali mwana wa chipembere, posakhalitsa anayamba kusewera ndi Enkare, mwana wa njati.

Amayendera limodzi kuli konse.

10

Usiku wina, onse anadzutsidwa ndi kufika kwa Ambia.

11

Ambia anali wa miyezi isanu.

Anali wofooka atayenda ulendo wawutali.

12

Chifukwa cha khosi lake lalitali, Msungi anakwera mmwamba ndi botolo la mkaka kuti ammwetse Ambia mosavuta.

13

Timapasa tiwiri, Abei ndi Moit, tinafika mkatikati mwa mwezi wa Ogasiti.

Awa anali ana a gwape omwe anali a maola ochepa. Anali akudwala kwambiri.

14

Aliyense anali ndi chisoni Abei atafa patatha sabata imodzi.

Koma Msungi ndi womuthandiza anapulumutsa Moit.

15

Ana anyama amasiye womalizira kufika mwezi wa Ogasiti anali Kopi, Kepi ndi Keji.

Ana a mkango amenewa anali ndi masabata awiri. Anafika ali ndi njala kwambiri.

16

Msungi ndi womuthandiza amakonda nyama zonse, ndi zosamvera zomwe.

17

Mwana wosamvera kwambiri anali Lobolia.

Lobolia amakonda kubisa mandala a Msungi.

18

Anthu onse ogwira ntchito pa malopa amalimbikira kulera ana a nyama.

Amayembekezera kuti tsiku lina ana wonse amasiye adzaima paokha. Kenako, adzabwerera kuthengo.

19

Zili ndi zaka zingati ndipo zilipo zingati? Werenganinso nkhaniyi ndipo muyankhe mafunso awa.
1. Ndi nyama zingati zomwe zinafika ku malowa mmwezi wa Ogasiti?
2. Anafika moyambirira mwezi umenewo ndi ndani?
3. Kodi nyama imeneyi inali ndi zaka zingati?
4. Anafika momalizira ndi ndani?
5. Ndi nyama ziti zazing'ono zomwe zinafika momalizira?
6. Zinali ndi zaka zingati?
7. Ndi nyama iti yayikulu yomwe inamalizira kufika mwezi wa Ogasiti?

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Msungi ndi nyama za masiye
Author - Nina Orange
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Magriet Brink
Language - Chichewa
Level - Longer paragraphs