Dezi wodabwitsa
Nozizwe Herero
Siya Masuku

Kalekale, panali kamunda pafupi ndi kamudzi kena.

1

Pamakhala kankhuku kotchedwa Dezi.

2

"Ndikadzakula, ndimafuna kudzauluka m'mulengalenga," Dezi anatero.

3

Nkhuku zinzake zonse zinamuseka.

4

"Ndiwe wodabwitsa zedi," zinatero. "Sitidzasewera nawenso."

5

"Dezi, tingathe tonsefe kukupiza mapiko athu koma ndikovuta kwambiri kuti nkhuku ziuluke." Mayi anamuwuza.

6

Dezi analimbikirabe. Tsiku ndi tsiku, amayesera kukupiza mapiko ake. Kupi! Kupi! Kupi! Anayesera kukupiza mapiko ake koma analephera kuuluka.

7

Akamayesera kuuluka, amaganizira atauluka mlengalenga, akuyang'ana nkhuku pansi. Amaganizira atauluka kuposa achacha ndi ananzenze. Mbalame zikudabwa, "Aaa! Nkhuku yowuluka"

8

Ndiye kunali kupi! Kupi! Kupi! Tsiku lililonse Dezi amakupiza, mapiko ake.

9

Amatha kunyamuka ndithu koma kenako amagwanso pansi.

10

"Sindidzathadi kuwuluka! Dezi analira kwa mayi ake. "Nkhuku zina zija zimanena zoona."

11

"Dezi, ndiwe wosiyana ndi nkhuku zinazi. Sizimafuna kuwuluka koma iwe umafuna! Ungathe," mayi anatero.

12

Mawa lake, Dezi anakwera pa mwamba pa khola la nkhuku ndi kukupiza mapiko ake. Anawuluka mlengalenga, anakupiza mapiko ake, kupi! Kupi! Kupi! Kenako...

13

Phwafaaa!

14

Nkhuku zina zija zinaseka mokweza. "Ha ha ha! Tidakuuza iwe! Nkhuku sizingathe kuuluka"

15

Koma tsiku lotsatira, Dezi anakwera pamwamba kwambiri, pothera pa denga la nyumba. Kupi! Kupi! Kupi! Dezi anakupiza mapiko ake.

16

Anauluka mlengalenga akukupiza mapiko ake. Anakupiza ndi kukupiza mapiko ake.

17

Anapitiliza kuuluka! Mphepo pansi pa mapiko ake inakankha mwamphamvu ndipo anauluka mlengalenga kuposa kale. Achacha ndi ananzenze anati, "Zodabwitsa! Nkhuku youluka!"

18

Nkhuku zina zinafuna zitakhala ngati iye.

19

Zinati, "Ooo Dezi, ndiwe wodabwitsa."

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Dezi wodabwitsa
Author - Nozizwe Herero
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Siya Masuku
Language - Chichewa
Level - First paragraphs