Daisy Odabwisa
Nozizwe Herero
Siya Masuku

Kalekale pamunzi wina.

1

Panali kankhuku kocedwa Daisy.

2

"Ine nikakula, nifuna kuuluka mumwamba kufika kumlengalenga," anati Daisy.

3

Koma nkhuku zonse zinamuseka Daisy.

4

"Iwe ndiwe osokonezeka," zinati nkhuku zina. "Ise tizaleka kusowela na iwe."

5

"Daisy, tingakwanise kupukusa mapiko koma nicovuta kwambili kuti nkhuku iuluke," anati amake Daisy.

6

Koma Daisy sanaleke kuyesa. Masiku onse anayesesa mobwezelabwezela payeka, kupukusa mapiko ake. Puku, puku, puku, anapukusa mapiko ake koma sanakwanise kuuluka.

7

Pamene anali kuyesesa mobwezelabwezela anayelekeza kuti alikuuluka mumwamba mumulengalenga apenyelela nkhuku pansi pake. Daisy anayelekeza kuti auluka kupitilila mbalame. "Taonani!" Mbalame zinati, "Onani nkhuku ikuuluka"

8

Puku, puku, puku masiku onse Daisy anapukusa mapiko ake.

9

Daisy akakwanisa kunyamuka anali kugwa ntawi zonse.

10

"Siningakwanise kuuluka," Daisy analila nauza amai ake. "Anzanga akunena zoonadi."

11

"Daisy iwe usiyana na nkhuku zina. Iwe ufuna kuuluka, nkhuku zina sizifuna kuuluka! Iwe ungakwanise," anati amake Daisy.

12

Siku losatila Daisy anakwela pamwamba pa khola, puku,puku,puku anapukusa mapiko ake. Anauluka mumpepo ndipo anapukusa, napukusa, napukusa mapiko ake posatila pake……

13

PHWE…

14

Nkuku zina zinaseka kwambili. "Ha ha ha! Nkuku sizingauluke!"

15

Koma siku losatila, Daisy anakwela pamwamba kwambili, pamwamba pa nyumba. Puku, puku, puku, Daisy anapukusa mapiko ake.

16

Daisy anauluka napukusa, napukusa, napukusa mapiko ake posatila pake…..

17

Anapitiliza kuuluka! Mpepo pansi pamapiko ake inapita na mphamvu ndipo Daisy anauuluka kupita mumwamba! Mbalame zinati, "Chodabwisa! Nkhuku ikuuluka!"

18

Nkhuku zonse zinafuna kukhala ngati Daisy.

19

Nkhuku zinati, "Taonani Daisy ndiwe odabwisa!"

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Daisy Odabwisa
Author - Nozizwe Herero
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Siya Masuku
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs