Kudabwa kwa mwana wa njovu
Judith Baker
Wiehan de Jager

Tonse tiziwa kuti njovu ili na citambi citali.

1

Koma paciyambi, citambi cinali cifupi ndiponso conenepa.

2

Pamene anabadwa mwana wa njovu, zina lace Dabwani, anali na funso ku nyama iliyonse.

3

Anadabwa pa utali wa nyamalikiti. Dabwani anafunsa, "Kodi cifukwa ninji nyamalikiti ali na mukosi utali?"

4

Dabwani anadabwanso pomwe anaona cipembele. Anafunsa kuti, "Kodi cifukwa ninji nyanga yako niyokutwa?"

5

Dabwani anadabwanso pomwe anaona mvuu. Ndipo anafunsa kuti, "Cifukwa ninji uli na maso ofilila monga moto?"

6

Ndipo anadabwanso pomwe anaona ng'wena. Dabwani anafunsa, "Kodi ng'wena umadya cani mumazulo?"

7

"Maloza! Usakabwezepo kufunsa funso iyo!" anamucenjeza amai ake. Dabwani anacokapo wokumudwa.

8

Mofulumila, Kwalala ocenjela anauza Dabwani, "Nilondole kumsinje nikakuonese cakudya cakumazulo cang'wena."

9

Ndipo Dabwani analondola Kwalala kumsinje.

10

Dabwani anasakila mumpepete mwa msinje. Anayangana mu mazi nafunsa, "Kodi cakundya camumazulo cako nicani?"

11

"Bwanji?," mwala wa mumpepete mwa msinje unapeleka moni. Dabwani anayanka nati, "Bwino." Dabwani anafunsa, "Kodi cakudya camumazulo cang'wena nicani?"

12

"Welama nikuuze," unayanka mwala. "Pitiliza kuwelama." Dabwani anawelamisa.

13

Gwii! mpuno yake inagwiliwa na mano yangw'ena. "Waciona! Lelo uzakala cakudya cakumazulo cang'wena," anatelo Kwalala.

14

Dabwani anakala pansi nadonsa mwa mpamvu mpuno yace. Koma ng'wena anagwilisa.

15

Citamba ca Dabwani cinadonseka ndipo cinatalimpa kwambili. Thii! Dabwani anagwa pansi.

16

Ndipo ng'wena ina bwelela mumazi mwaukali kamba kolepela kugwila cakudya camumazulo.

17

Dabwani anayangana citamba cace. Koma sanaone mapeto acitamba cace.

18

Citamba cace cinatalimpa kotelo kuti anakwanisa kutyola zipaso mu mitengo yitali.

19

Ndipo anakwanisa kuzitila mazi patupi lace lonse zuwa litatenta. Kufikila lelo njovu zonse zili na zitamba zitali.

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kudabwa kwa mwana wa njovu
Author - Judith Baker, Lorato Trok
Translation - Lusaka Teachers
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - First sentences