Uyu ni Cona.
Uyu ni Galu.
Galu na Cona akala munyumba imozi.
Nyumba ili na komo na sindwi.
Cona na Galu ali na mpila.
Mpila uli na utoto wofilila, wobiliwila na wamsipu.
Cona na Galu asewela na mpila. Cona aponyela Galu mpila.
Galu agwila.
Galu naye aponyela Cona. Cona agwila mpila.
Ndipo Cona anaponya mpila mumwamba kwambili.
Ah! Ah!
Mpila uli pa sindwi ya nyumba.
Cona na Galu anaona mpila pa sindwi ya nyumba.
Cona na Galu analepela kutenga mpila pa sindwi ya nyumba.
Ndipo anayamba kulila.
Njovu yikulu yinabwela.
Njobu yikulu yinauona mpila pasindwi ya nyumba.
Njovu yinatenga mpila pansindwi napasa Cona na Galu.
Cona na Galu anasekelela.
Njovu yinamwetulila.
Cona, Galu na Njovu anayamba kumenya mpila. Cona anaponya mpila. Galu anagwila.
Galu naenso anaponya mpila. Njovu anagwila.
Njovu anaponya mpila kwa Cona ndipo Cona anagwila.
Sala bwino Cona.
Sala bwino Galu.
Sala bwino Njovu.
Onse anatelo.
Biblionef