Kusakila Mutima Wacisangalalo
Mosa Mahlaba
Selina Masego Morulane

Kuzizila kwampepo kunali kunapita ndipo zuwa inali kubwela mu muzi mwa Nkanyezi. Onkala mumuzi anali kubwela pamozi kuti asangalalile kubwela kwa zuwa. Nkanyezi anali kuyembekeza ici cisangalalao camuzuwa kupamabana siku lina lililonse mu caka.

1

Siku lina kuseni Nkanyezi anamvela akulu awili amumuzi akambilana za cisangalalo ici. "Antu a mumunzi wa Njovu analibe mutima wosangalala." "Kodi, tingankale naco bwanji cisangalalo ca zuwa ngati antu alibe mutima wosangalala," anafunsa akulu ena.

2

Nkanyezi anada nkawa. "Kodi zuwa lizapya bwanji ngati kulibe kuyimba kuti yiuke, kucosa tulo twa mpepo?" anazifunsa. Nkanyezi anaganiza kwa ntawi yai tali. "Nifunikila kupeza vamene tinasowesa," anaganiza Nkanyezi. "Nifunikila kupeza vintu vamene vizatandizila antu kufuna kusangalala mumuzi wanga."

3

Akulu akulu amumunzi anamupasa madaliso a pa ulendo. Anamupasa cola conyamulilamo vintu vamene azapeza pa ulendo. Nkanyezi anamvela manta koma anankala na cikulupililo kuti azagwila ncito iyi bwino bwino.

4

Nkanyezi anayenda usiku wonse. Anakwela ndipo anasika mapili. Anawoloka misinje zikulu. Anayenda mumadambo ndipo anafika ku citunzitunzi ca pili yofuwila.

5

Pamene kunayamba kufipa, Nkanyezi anafika mumunzi wamapatani na utoto wamene anali akalibe kuonapo. Nkanyezi anauza akulu akulu amumuzu uyu cilingo ca ulendo wake, cofuna kubweza mutima wacisangalalo kwa antu ake. Amai acikulile mumunzi anapasa Nkanyezi mpaso. Anati, "Mwacikodi tikupasa iyi penti kuti ingabweze utoto kumunzi wamene sutowa." Nkanyezi anakondwela ndipo ana onga akulu akulu, ndipo anaika penti mucola cake.

6

Kuseni-seni, siku lokonkapo, ananyamula cola ndipo anayambapo ulendo wake. Nkanyezi anayenda usiku wonse, anapita musanga yikulu yamene inali na vimitengo vitali vitali. Pamene kunafipa, anamvela ng'oma zili kulila. Anayenda mwamusanga-musanga, kuyenda kwamene kunali kulila ng'oma. Anamvela mpamvu zovina zili kubwela mumendo mwake ngankale kuti anali wolema.

7

Nkanyezi anazipeza mumuzi mwa Bubezi. Anapeza antu alinkale azungulila mulilo ndipo anali kuliza ng'oma na kuvina. Anauza akulu akulu amumuzi za ulendo wake wofuna kubweza mutima wa cisangalalo ku antu amumunzi mwake. Antu amumuzi mwa Bubezi anamupempa kuti apumule ndipo agone usiku umozi cabe.

8

Kuseni seni, mfumu inaitana Nkanyezi. "Mwana wanga," mfumu inati kwa Nkanyezi, "Nyamula ng'oma iyi. Ntawi iliyonse ukayiliza, ilila nyimbo yina yikalibe kulilapo." Nkanyezi anawonga akulu akulu amumunzi ndipo ananyamula ng'oma nayiika mu cola cake. Anayambapo ulendo wake. Anakondwela kwambili cifukwa ca mpaso iyi ya ng'oma.

9

Pasiku lacitatu la ulendo, anapita mu munda mwamene munali ng'ombe zoyiina ndipo anayamba kumvele kunyeleza mumpuno mwake. Anamvela kununkila ndipo anafunisisa kuyamba kudya, cifukwa anamvela mata mukamwa. Anakonka kafungo konunkila ndipo anapeza antu apika. Antuwa anali namapoto mwamene munali nyama zamene zinapikidwa bwino. Awa antu anali kuziwika kamba kamapikidwe ao. Nkanyenzi anali akalibe kudyapo vakudya vabwino monga ivi mu umoyo wake wonse.

10

Usiku unakonkapo, antu analikupika anapasa musikana uyu tonunkila toyika muvakudya twamene anali kuziba iwo cabe. "Iwe mwana watu," anati, "Nautu toyika mu vakuduya, antu onse, azadya vakudya nakukuta ndipo iyi siboza! Tikupasa mpaso ya vakudya." Nkanyezi anawonga akulu akulu amumunzi. Anaziwa kuti anali na vonse vamene anali kufuna. Anamvela mpamvu ndipo anayambapo ulendo wautali, wobwelela kumuzi kwao kwa Njovu.

11

Pamene anafika, antu anabwela pamozi kuti amvele mwamene anayendela. Anawauza nkani ya vintu vamene anaona na kumvela. Ndipo anasegula cola cake kuti awaonese mpaso zamene anapasidwa. Antu amumuzi anasekelela kwambili kulandila mpasozi. Mpaso za antu ena ndiponso kulimbikila kwa Nkanyenzi kunabwelesanso cisangalalo mumunnzi mwa Njovu.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kusakila Mutima Wacisangalalo
Author - Mosa Mahlaba
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Selina Masego Morulane
Language - CiNyanja
Level - Read aloud