Nonkungu Na Mbulu
Alan Kenyon
Wiehan de Jager

Kale kale kunali antu awili okwatilana ndipo anali osauka. Munyumba mwawo anali cabe na mwana umozi wamene anali kukondesesa zina lake inali Nonkungu. Pamene anakulako, makola ake anaganiza kuti ayende akankale na amalume ake olemela zina lao aMutonyama. Amai ake anamutungila vovala va bwino va maliboni, mabatani na ulungu. Sanalekezele apo, anamupangila na tokolobeka mu mukosi. Ndipo Nonkungu anayambapo ulendo woyenda kumunzi kwa amalume bake.

1

Pamene anaoloka cabe musinje, anapeza musikana avala magamba. "Uyenda kuti?" anafunsa musikana. Nonkungu anati, "Niyenda kwa amalume anga aMutonyama." "Cawama, aMutonya naine ni amalume anga, ndipo pamene uniona apa naine niyenda mukuceza kwao," anati musikana. Ndipo anayamba kuyenda pamozi. Pamene asikana anayenda ka ntawi kakang'ono, musikana anati kwa Nonkungu, "Mah! Vovala vako na vokolobeka vako nivabwino. Leka nivaleko."

2

Ndipo Nonkungu anavula vovala vake nopasa musikana. Nonkunga anadabwa cifukwa pamene musikana anavula vovala vake anapeza kuti musikana anali namucila! Ici cinamuyofya kwambili Nonkungu. Pamene anaona ivi, anaziwa kuti uyu musikana ni Mbulu. Pamene asikana anayenda pang'ono, Nonkungu anati "Nipase vovala na ulungu wanga."

3

Mbulu inayanka nati, "Nisiye nivale kufikila pa cimutengo paja." Pamene anafika pa cimutengo, Nonkungu anauza Mbula nati, "Mwamena tapanganilana, nipase vovala na ulungu wanga." Mbulu inayanka nati, "Nisiye nivale cabe tifike pa munda paja." Ndipo mwamanta, Nonkungu anavomela.

4

Pamene asikana anafika pa munda, Nonkungu anapempa Mbulu nati, "Nipase vovala na ulugu wanga." "Nisiye cabe nivala mpaka tifike pakanyumba kaja pamene azimai alinkale," anakamba Mbulu. Pamene anafika pa kanyumba, Mbulu ina kankila kumbuyo Nonkungu ndipo inatamangila kusogolo.

5

Mbulu inauza azimai anali pakanyumba nati, "Onani musikana uyu wavala magamba. Ankala anikonka zuba lonse. Nifunisisa kuti abwelele." Azimai anapindamuka nalangana Nonkungu. Nonkungu anayopa, ndipo anatawa nayenda kubisama kucibaya. Ndipo Mbulu inayenda kunyumba kwa amalume aMutonyama. Nanena nati, "Ine ndine mulisa wanu Nonkungu. Makolo anga anituma kuti nibwele ninkale naimwe."

6

A Mutonyama na banja lao anamulandila musikana uyo ndipo anamulangiza cikondi. Ananvesa cifundo Nonkungu cifukwa anagona mu cibaya ndipo anadya vakudya va agalu. Muzuba anabisama mu munda ndipo anayimba nyimbo yoti: "Maiwe navutika ine, maiwe navutika ine. Ananituma atate na amai kuti nikankale na amalume anga. Koma panjila ninakuma na Mbulu ndipo inatenga vovala vanga na ulungu wanga. Maiwe navutika ine, maiwe navutika ine."

7

Siku lina mwana wa aMutonya munyamata oyamba, anali kuyenda mu munda. Ndipo ananvela nyimbo yacisoni. Sanaziwe kuti nindani anali kuyimba nyimbo, koma pamene anafika kunyumba, anawauza atate ake vamene ananvela. A Mutonyama anayenda kumunda kukafufuza. Anamvela nyimbo ndipo anasakila-sakila mpaka anamupeza Nonkungu.

8

Nonkungu anauza amalume ake vonse vamene vinacitika. A Mutonyama anamutenga Nonkungu kumupeleka ku munzi ndipo anamubisa mu nyumba. Anaziwa vakuti acite bwino bwino kuti agwile Mbulu. A Mutonyama anali kuziwa kuti mucila wa Mbulu ukondesesa mukaka. Ndipo Mbulu singapitilile mukaka cosafuna kumwa. Ndipo aMutonyama anatuma antu awo kuti akumbe mugodi ukulu wamene anazulisa na mukaka.

9

A Mutonyama anaitana asikana onse amumunzi kuti abwele atengeko mbali mumasowela ojumpa. Mbulu anavutika cifukwa sanali kufuna kuti ajumpe mugodi. Anaziwa bwino bwino kuti mucila wake uzamvela njota yofuna kumwa mukaka. Ndipo anayenda munyumba namangilila nampavu mucila wake kumubili wake. Pamene anasiliza anayenda kunkala na anzake kuti atengeko mbali mu masowela.

10

Asikana anajumpa mugodi wa mukaka umozi na umozi. Ntawi inafika yakuti naye Mbulu ajumpe. Anayesesa kuti ajumpise mumwamba koma mucila wake unamasuka. Mucila wa Mbulu unamudonsela pansi mpaka anagwela mumukaka.

11

Pamene Mbulu inali ku palakata-palakata, anyamata anayamba kufwikila mugodi na micenga mpaka mbulu inafwikilika. Nonkungu anankala na amalume ake okondwela kwantawi yayitali.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nonkungu Na Mbulu
Author - Alan Kenyon, Viv Kenyon
Translation - Bether Mwale Moyo, Vision Milimo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - Read aloud