Kulimba mutima kwa Nangila
Violet Otieno
Vusi Malindi

Kale kale, kunali munyamata amene anali na cilonda cikulu pa kwendo. Sanali kuyenda kapena kuiimilila. Munyamata uyu anali kunkala na mukazi wake na ana ake.

1

Mucikwati cao anali na ana amuna atatu namukazi umozi. Mwana mukazi zina lake Nangila ndiye anali kusunga atate ake. Ana amuna anali alimi ndipo anali kudyesela vinyama.

2

Nangila anali musikana wokongola kwambili. Antu amumuzi onse anali kumukonda nakumupasa ulemu. Makolo ake anali kumufunila mwamuna wabwino. Pakuti apeze mwamuna wolemekezeka, anapasa cocita covuta kwa wamene anali kufuna kumukwatila Nangila.

3

Wamene anali kufuna kukwatila Nangila anali kufunika kubwelesa mankwala amene anali mukati mwa musinje, wamene unali pafupi na munzi. Mankwala aya anali kufunikila kupolesa cilonda ca atate ake Nangila. Koma mumsinje uja munali mozula mizimu zoyofya.

4

Amuna ena anayesako kutenga mankwala koma anakangiwa. Amuna ena anakangiwa nakubwelako ku musinje.

5

Nkani iyi inamudesa nkawa Nandila. Abale ake amuna anali kukangiwa kuyenda ku musinje. Anazipeleka kuti akasakile aya mankwala eka. Amai ake anati, "Mwana wanga ona mwamene anakangiwila amuna ampamvu, iwe ndiwe wamene ungakwanise?" Koma Nangila anazipeleka.

6

Paulendo waku musinje, Nangila anapeza ka nkalamba kananyamula nkuni. Nangila anakatandiza kunyamula citundu ca nkuni. Aka ka nkalamba kanayamika kwambili kanati kwa Nangila, "Nizakuuza mwamene ungafikile ku musinje wa mizimu, navocita ukafika kuja."

7

Pamene anafika pa musinje, Nangila anaona mizimu za mu banja mwake zikumwa manzi nakuvina. Musikana anayembekeza naku penya, mpaka mizimu zonse zinagona tulo.

8

Pamene mizimi zinali gone, Nangila anaziponya pamanzi. Anapeza mankwala ndipo anayika mucola cake. Pamene anali kuoloka kubwelela, mafunde apamanzi anaima kumuzungulila.

9

Mizimu zinauka. Pali iyi ntawi, anaimba kanyimbo kamene kankalamba kanamupunzisa: Ine, ndine mwana wa Wekesa, Nabwela cifukwa amuna ayopa kwambili kubwela. Atate afuna mankwala aya kuti yakapolese cilonda cao. Ndiye cifukwa napezeka kuno. Mumalo yamene ambili ayopa kufika. Cifukwa mizimu nimfumu.

10

Nangila anali na lizu labwino anayimba ndipo mizimu zinamupempa kuti abwezele, nobwezela nobwezelanso kuimba. Pamene anali kuimba, mizimu zinabwelela mutulo. Nangila anatawa luwilo lodabwisa mpaka pamene anafika mu muzi.

11

Antu onse anali kuyembekeza Nangila. Pamene anasiliza kusewenzesa mankwala apa musinje, atate ake anayambanso kuyenda. Munzi onse unayamba kupasa ulemu nakumuonga Nangila.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kulimba mutima kwa Nangila
Author - Violet Otieno
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Vusi Malindi
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs