Mfumu Kayanja namwana wake musikana
Amana Yunus
Natalie Propa

Kale kale kunali mfumu zina lake Kayanja. Mfumu inali ku nkala mu nyumba ya mafumu na amai mfuni, na mwana mkazi zina lake Apenyo. Apenyo anali wokongola kwambili ndipo antu onse anali kufuna kumukwatila. Koma amfumu anatomolo cimalo cikulu kwambili.

1

Pafupi na nyumba ya amfumu Kayanja kunali kunkala amfumu amene anali kuitanidwa kuti Aludah waMukulu. Anali kuwaita kuti 'waMukulu' cifukwa kwamene anali kunkala onse antu anali kuwalemekeza. (Sanalikufuna masobela!) Sipanapite ntawi pamene amai mfumu Aluda anamwalila na malungo, ndipo a mfumu anali kufuna kukwatilanso.

2

Ndipo mfumu Aluda, oiina ndiponso nkalamba, anayenda kulipila ndalama yacimalo kuti akwatile mwana wamfunu. Pamene azibambo analikukambilana nkani ya cimalo, wancito wina zina lake Kakembo anali kumvela vamene anali kukamba. Kakembo anali kumvelana kwambili na mwana wa mfumu Apenyo.

3

Amfumu Aludah anavomela kugawa pakati cuma cao kuti alipilile cimalo. Kuikilapo na nsingano yotungila yamene inalikufunikila pa cimalo. Kukonzekela kwa ukwati wa amfumu Aluda na Mwana wa mfumu Apenyo kunacitika mwacisinsi. Amfumu anaziwa kuti mwana wao sazakondwela na cikwati ici.

4

Sabata limozi kuti ukwati wakumafumu ucitike, wancito Kakembo anayenda kwa Apenyo. "Mwana mukazi wamfumu, atate ako, akukonzekela ukwati na amfumu Aludah wamene uzankalako sabata libwela," anati Kakembo.

5

Apenyo mwana wamfumu anakalipa kwambili ndipo poyamba navocita vinamusowa. Ndipo anaganiza nati, "Siningakwatile amfumu Aluda aja ankalamba oiina. Kulibe! Nifunika kuyenda kwa Trevor nione vamene angacite nikalibe kucedwa." Trevor anali bwenzi wa Apenyo.

6

Usiku umenewo, Apenyo anatawa kucoka mu nyumba ya mafumu. Atate ake ngati anaziwa kwamene anali kuyenda, ngati anakalipa kwambili. Anatawa, kupita musanga lalikulu mofipa. Anapita pa myala napa vimitengo, mpaka anafika kwa Trevor wake. Pamene anafika ku nyumba yake, anali wolema, na njala ndiponso na njota.

7

"Okondedwa wanga, nanga nicani watamanga mutunda utali uyu weka iyi ntawi ya usiku?" anafunsa Trevor. Trevor anakangiwa kunkazikika pamene anayembekeza kuti Apenyo ayambe kukamba.

8

"Mwana mukazi wamfumu, kodi vuto nicani?" anafunsa Trevor. Apenyo anapeema ndipo mwacisoni anati, "Atate afuna kunikwatilisa kwa aMfumu Aludah waMukulu. Siningakwatile aja ankalamba oiipa. Trevor, nifuna kukwatila iwe ngankale kuti ndiwe mpawi. Nilibe vuto nakuvutika. Ine nikukonda."

9

"Manje mwana wamfumu, ine nilibe ndalama zolipilila cimalo, uziwa kuti ndine munyamata osauka." analila Trevor. Apenyo anayanka nati, "Niziwa koma ndiwe weka wamene nifunika kukwatiliwako." Anaganiza ntawi yaing'ono, "Tiye kuli Kategga kuti atitandize kuoloka musinje mu wato yake, kuti titabe. Ndipo atate sazakatipeza."

10

Ku nyumba yamafumu, mfumu Kayanja inaziwa kuti Apenyo panalibe ndipo inauza antu kumusakila mumunzi onse. Akapaso a amfumu, masilikali na ena onse anasakila koma sanamupeze Apenyo.    Antu awa anabwelela kwa amfumu ndipo anawauza amfumu kuti Apenyo sanaoneke. "Kansi bwelelani musanga mukasakile," anati amfumu Kayanja. Amfumu anakalipa kwambili.

11

Pamene Apenyo na Trevor anali kuyenda kumusinje motamanga, makumbi ofipa anayamba kukumana mumwamba. Cimvula cacikulu cinali pafupi.

12

Kategga anali kumangilila ma wato ake pamene Apenyo na Trevor anafika. Trevor anapempa Kategga kuti awaolose musinje. Kategga anakana, anati cimvula cikulu cinali kubwela ndipo cingabwelese mavuto pa manzi.

13

Trevor analimbikila ndipo anauza Kategga cilingo camene anali kufunila kuoloka musinje. Ndipo anangenesa kwanja mutumba, nacosamo ndalama napasa Kutegga. Pamene Kategga anamvela nkani yao, naona ndalama, anamvela cifundo. Anavomela kuwaolosa musinje, ngankale mwamene kunali kuonekela kumwamba.

14

Kategga anadonsa wato ndipo anauza Apenyo na Trevor kuti angene mukati. Ndipo anayamba kuyendesa wato, kuoloka musinje. Pamene mfumu Kayanja na mfumu Aludah anafika kumusinje, anaona antu atatu muwato ndipo anaziba kuti Apenyo na Trevor anali kutawa.

15

Cimpepo cinayamba kunyang'anisa wato ndipo Kategga anakangiwa kuti a longosole. Amfumu Kayanja anakuwa nati, "Apenyo, napapata bwela! Nakukululukila. Sinizakakupasa cilango cili conse iwe ndiponso Trevor." Koma anacedwa. Wato inapindamuka ndipo antu atatu anali mukati anagwela mumanzi. Onse antuwa anamwela. Kucokela apo, antu onse mumunzi mwa amfumu Kayanja anayamba kukwatila muntu wamene anakonda ngankale niwolemela ngankale niwosauka.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mfumu Kayanja namwana wake musikana
Author - Amana Yunus
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Natalie Propa
Language - CiNyanja
Level - Read aloud