Mfumu Yambalame
South African Folktale
Wiehan de Jager

Kale kale, mbalame zinali na musonkano. Zinali kufuna mfumu monga antu navinyama. Kodi ni mbalame iti yamene iyenela kunkala mfumu?

1

"Nkwazi. Niyampamvu ndipo iyenela kunkala mfumu," inati mbalame imozi. "Kulibe, Nkwazi akaitana amveka ngati ali namadandaulo," inati mbalame ina. "Koma Ntiba-Tiba! Cifukwa iye niwamukulu kwambili ndipo amawuluma ngati Mukango," inati mokuwa mbalame ina. "Yayi! Sakwanisa kumbululuka uyu ndipo mfumu ya mbalame iyenela kukwanisa kumbululuka."

2

"Ndine niyenela kunkala mfumu, cifukwa ndine okongola," inati Nkangalukuni, nanyamula mucila wake. "Uzikonda kwambili iwe," anati Kazizi. "Ine nili namenso yakulu kwambili kupambana mbalame zonse, ndine niyenela kunkala mfumu. "Osati iwe!" zinakuwa mbalame zina. "Ugona iwe zuba ikacoka!

3

Zisanafike kutali kusanka mfumu, mbalame yina, inankala naganiza. "Iyo mbalame yamene izakwanisa kumbululuka kuyenda kumwamba kwambili, kusiya mbalame zonse ndiye yamene izankala mfumu," inakamba mbalame yina na lizu laling'ono ngati la musikana. "Inde! Inde!" mbalame zonse zinavomeleza ndipo zonse mbalame zina mbululuka kuyenda kumwamba kumulengalenga.

4

Sekwe anambululuka siku limozi cabe noyenda kufika pamwamba pamalupili yatali kupambana mapili yonse yamuziko. Nkwazi anambululuka masiku awili nokafika mumuleng-lenga pamwamba pamapili. Koma Kubi anambululuka kwamasiku atatu cosa imilila, anambululukila kuyenda kuzuwe. Pamwamba mbalame zinamvela Kubi akuwa. "Ndine nili mumwamba, ndine mfumu!"

5

Kubi anamva pamwamba pake mau akuti, "Tii, tii, tii! Ndine nili mumwamba kwambili, ndine mfumu." Aka kanali Katyetye, kambalame kakang'ono pambalame zonse. Katyetye kanagwililila papiko likulu la Kubi. Nthawi imene anali kumbululuka Kubi kuyenda mumwamba mumulengalenga.

6

"Suzanipitililanso," ananena Kubi. Ndipo anayangana mumwamba nombululuka kuyendelako mumwamba na mumwamba. Nambuluka nombululukilako kumwamba mpaka kumbululuka kwake kunafika posilizila. "Nili mumwamba kupambana mbalame zonse! Ndine mfumu yanu," anakuwa Kubi.

7

Koma munyansi mwa papiko la Kubi munali munagwililila ka mbalame kakang'ono. "Tii, tii! Tii, tii! Ndine, ndine mung'ono, ndine mfumu wanu." Kubi analema ndipo anakangiwa kumbululukilako kumwamba.

8

Ndipo anambululukila pansi Kubi, nayenso Katyetye anagwililila papiko la Kubi. Mbalami zinakalipila Katyetye nayembekeza kuti bamunyule mangala Katyetye.

9

Pamene anaona mwamene zinakalipila Mbalame zina, Katyetye mwamusanga-musanga ana mbululukila mumugodi munalibe Njoka. Mbalame zinali kuyembekezela zinalema. Ndipo zinauza Kazizi nati, "Iwe uli namenso yakulu uyembekeze apa pamugodi kuti akachoka Katyetye umugwile." Ndipo Kazizi anankala pa mugodi.

10

Koma zuba inapya ndipo patapita ntawi ing'ono, Kazizi anagona. Katyetye anasonjela naona kuti Kazizi aligone, ndipo anacoka nombululukila kumwamba kutali.

11

Cifukwa Kazizi analekelela Katyetye kuti atawe, Kazizi anagwidwa na nsoni. Ndipo kucokela apo, Kazizi asakila cakudya cake usiku cabe.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mfumu Yambalame
Author - South African Folktale
Translation - Bether Mwale Moyo, Vision Milimo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - Read aloud