Cuti kwa Ambuya
Violet Otieno
Catherine Groenewald

Udongo na Apiyo anali kunkala mu tauni na atate awo. Anali kukonda ntawi yamene masikulu anali ovala, cifukwa anali kuyenda pacuti kwa ambuya awo. Ambuya awo anali kunkala mu muzi wa pafupi na musinje waukulu.

1

Udongo na Apiyo anali okondwela cifukwa inali ntawi yoyenda pa cute kwa ambuya awo. Usiku analonga vyola vawo kukonzekela ulendo. Usiku uyo, ana awa, anakangiwa kugona ndipo anaceza usiku onse pazaulendo.

2

Kuseni seni anayambapo, ulendo woyenda kumunzi mu motoka ya atate awo. Anapitilila mapili, vinyama vamusanga ndiponso minda za masamba. Ana awa, anawelenga mamotoka munjila ndipo anayimba nyimbo.

3

Panapita ntawi ndipo ana awa anagona cifukwa analema.

4

Pamene anafika pa munzi, atate a Odongo na Apiyo ana usa ana. Ana anapeza ambuya awo aligone pa mpasa munsi mwa mutengo. Ambuya awo anali muzimai wampamvu, ndipo wokongola kwambili.

5

Ambuya anakondwela kwambili ndipo anavina vina, nayimba nyimbo zacisangalalo. Azukulu nawo anakondwela kwambili, ndipo anapasa ambuya awo mpaso zomwe anawabwelesela. "Yambililani kusegula yanga mpaso," anati Odongo. "Yambililani yanga," anati Apiyo.

6

Pomwe anasegula mpaso, Ambuya awo anawadalisa azukulu awo monga mwa mwambo.

7

Ndipo Odongo na Apiyo anayenda panja nayamba kupilikisa ma bulaula na mbalame.

8

Ana awa, anakwela mitengo ndipo anasewela na manzi.

9

Pamene kunafipa, ana anabwelela kunyumba mukudya cakudya ca usiku. Koma ana awa anagona akalibe kusiliza kudya.

10

Mumawa mwake, atate ake a Odongo na Apiyo anabwelele ku tauni. Ana anasala na ambuya awo.

11

Odongo na Apiyo anatandiza ambuya awo na zincito za panyumba. Ana awa anatapa manzi na kusakila nkuni. Anadoba mazila ndipo anatyola ndiyo mumunda.

12

Ambuya anapunzisa azukulu awo kupika nsima, nsomba, na ndiyo zina zakumunzi.

13

Kuseni kwina, Odongo anayenda kudyesela ng'ombe. Ng'ombe zina zinayenda mumunda mwa antu ena. Antuwa ankalipa kwambili ndipo ananena kuti azazigwila ng'ombe. Odongo ana punzila, ndipo anatayako nzelu kuti Ng'ombe zisazipanga milandu.

14

Siku lina ana anayenda ku musika na ambuya awo. Anayenda kukagulisa ndiyo za mumunda, shuga na sopo. Apiyo anali kukonda kuuza antu mitengo za vintu. Odongo anali kukonda kulongeza vintu vamena antu anali kugula.

15

Pakusila kwa siku ana anatandiza ambuya awo kuwelenga ndalama, ndipo pamozi anamwa tiyi.

16

Mwazizizi, masiku yonkala pa cute yanasila ndipo ana anafunika kubwelela ku tauni. Ambuya anapasa Odongo kapu ndipo anapasa Apiyo covala ca mpepo. Ambuya analonga cakudya capaulendo.

17

Odongo na Apiyo sibanafune kubwelela ku tauni. Ana anapempa ambuya awo kuti ayende nawo ku tauni. Koma ambuya anati "Ndine nkalamba ndipo siningankale mu tauni, koma mukabwela kuno kumuzi muzakanipeza."

18

Odongo na Apiyo analayilana na ambuya awo.

19

Pamene Odongo na Apiyo anabwelele ku sukulu, anauza anzao za umoyo wakumunzi. Anzao ena anakonda umoyo wamu tauni koma ena anakonda umoyo wakumunzi. Koma onse ana ananena kuti ambuya a Odongo na Apiyo ni abwino mutima.

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Cuti kwa Ambuya
Author - Violet Otieno
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Catherine Groenewald
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs