Nkuku yamupita kunzelu Nkwazi
Nathan Higenyi
Rob Owen

Kale kale Nkuku na Nkwazi anali abwenzi. Siku lina, Nkwazi inapeza Nkuku yaimilila na kwendo imozi munyansi mwa mutengo icokela kugula vintu vosiyana siyana.

1

"Nanga iwe kwendo yako imozi wapeleka kuti?" inafunsa Nkwazi.

2

Nkuku inayanka nkwazi nati, "Nasintanisa kwendo yanga na vintu ivi." Ogulisa wajuba kwendo yanga ndipo anipasa katundu iyi nilinayo.

3

Nkwazi anakumbwila ndipo anafunsa Nkunku ngati naye angadulise kwendo. Cifukwa analikukonda tuntu twabwino twamumasitolo. Kosataya ntawi, Nkuku inati kulibe navuto olo limozi.

4

Nkwazi anayenda kwa ogulisa mu sitolo napempa kuti amudule kwendo. Pambuyo pake, asintanise kwendo na zintu zamusitolo.

5

Ndipo Nkwazi inayambapo kuyenda kunyumba chogonta, koma, inasekelela mukati mwa mutima, cifukwa ogulisa mu sitolo anamupasa vintu vamene anali kufuna.

6

Mwacisoni, pamene Nkwazi anafika kunyumba anapeza nkuku ili na mendo yake yabili yokwanila.

7

Ici cinamukalipisa Nkwazi, ndipo ananyamuka kuti agwile na kumenya Nkuku koma sanakwanise cifukwa Nkuku inataba. Cifukwa cokangiwa kugwila Nkuku, Nkwazi inayamba kusakila sakila nakugwila tubana twa Nkuku. Kufikila lelo, Nkwazi amadya tubana twa Nkuku.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nkuku yamupita kunzelu Nkwazi
Author - Nathan Higenyi
Translation - Bether Mwale Moyo, Vision Milimo
Illustration - Rob Owen
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs