Mwamene Kanyelele Kanapulumusila Nkunda
Kholeka Mabeta
Wiehan de Jager

Zuba inali inapya ndipo kunali koyuma musanga.

1

Kanyelele sikanamwepo manzi masiku yapitapo.

2

"Nifuna tumanzi tung'ono cabe olo kuti nitokugwa kumatepo," kanati Kanyelele.

3

Koma kunayumila kumozi na mame.

4

"Ngati sinizamwa manzi, nizafa," kanalila Kanyelelele. "Nifunikila niyende kumusinje wamene ninamvelapo."

5

"Musinje niwozula ndipo uli na mpamvu, uzakudonsa," anati Kamundi wanzelu.

6

Koma Kanayelele kanali nanjota kwambili. "Nizafa ngati sinikumwa manzi." Ndipo Kanyelele kanayenda mukusakila manzi.

7

8

Kanapita pa vimauzu na pavinkuni voyuma.

9

Kanayenda mpaka kanamvela congo ca manzi. Unali ni musinje! Kanamvela mafunde ya manzi.

10

Kanyelele kanamwa manzi yozizila.

11

Kanakondwela kwambili ndipo sikanamvele mafunde pamene yanali kubwela.

12

Kanyelele kanayesa kugwila mauzu yamene yanali kuyangalala pafupi pake. Koma manzi yanakakanka ndipo kanadonsewa na manzi.

13

''Nitandizeni! Nitandizeni!" Kanaitana."

14

''Mwamusanga-musanga, kwela apa," inati Nkunda yotuba, yagwililila kamutengo mukamwa mwake."

15

16

"Nizankala pano kuti nionge zikomo kwa Nkunda," Kanyelele kanaganiza. "Nizayembekeza mpaka abwele kumwa manzi Nkunda." Koma Nkunda sanaonekele.

17

Siku lina pamene Kanyelele kanali kuyembekeza Nkunda, anyamata awili anabwela ku musinje. Anyamata awa anali na malegeni.

18

''Kuli Nkunda yotuba yamene imabwela kuno mukumwa manzi," anati munnyamata umozi. "Lelo usiku tizayidya.

19

20

''Sinizalekelela anyamata awa kuti apaye Nkunda yotuba," kanaganiza Kanyelele."

21

Pamenepo, Nkunda yotuba inambululuka kubwela pansi kuti imwe manzi.

22

23

Kanyelele kanaganizila vocita.

24

Kanajumpila pa kwendo kwa munyamata umozi. Kanyelele kanaluma munyamata uja nampamvu zake zonse.

25

Munyamata anajumpa. Ndipo anakuwa nati, "Maiwe! Maiwe!"

26

Nkunda yotuba ndiye mwamene ina tilimukila ndipo inambululuka. Ndiye mwamene inapulumukila.

27

Ndiponso ndiye mwamene Kanyelele kana ongela Nkunda yotuba cifukwa co pulumusa umoyo wake.

28
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mwamene Kanyelele Kanapulumusila Nkunda
Author - Kholeka Mabeta, Judith Baker
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - First sentences