Awa ndi a Agnes. Iwo ndi aphunzitsi anthu.
Iwo amagwiritsa nchito ndodo poyenda.
Uyu ndi Malizani. Iye ndi wanyimbo zanga za pamtima za pawailesi.
Malizani ali ndi vuto la maso, sapenya.
Awa ndi a Mariya. Timakhala pafupi nawo kumene timakhala. A Mariya ndi mlimi.
A Mariya ndi a gonthi, samamvera.
Uyu ndi Sitefano. Ameneyu ndiye aposa anyamata ena onse polowetsa zigoli m'masewera a mpira.
Sitefano alibe manja, koma agolesa kwambili mu gulu latu la a mpira.