"Bwanji?" Kalulu anapatsa moni fulu. Kalulu anauza Fulu kuti acite mpikisano othamanga ndipo iye anavomera. Iwo anasankha bulu kuti akhale ogwira nthambo.
M'mamawa kutacha anayamba mpikisano wao ndipo bulu anagwira ndembera kuyambitsa mpikisano.
Pomwe bulu analiza wezulo Kalulu anathamanga kwambiri kusiya Fulu.
Kalulu podziwa kuti fulu wakhalira, anapumula pa mtengo ndipo pamenepo tulo tunamugwira nagona. Fulu atafika pamenepo anaona kuti Kalulu wagona ndipo iye anapitiriza ulendo.
Pomwe kalulu anauka anaona mapazi a Fulu kuti wapita kale. Kalulu anathamanga kwambiri koma sanamupeze fulu ai.
Kalulu anapeza kuti fulu adutsa panthambo pothera. Kalulu analuza mpikisano othamanga.