Nkuku na Bongololo
Winny Asara
Magriet Brink

Nkuku na Bongololo anali abwenzi. Koma anali kukonda mupikisano mumasowela. Nkuku na Bongololo anayamba kumenya bola yamendo kuti aziwe wamena anali kuziwisisa kumenya bola.

1

Nkuku na Bongololo anayenda kubwalo lomenyela bola ndipo anayamba kumenya bola. Nkuku inali kutamanga koma siyinasiye bongololo. Nkuku inamenyela kutali bola, koma kamenyedwe ka Bongololo kanapitilila kamenyedwe ka Nkuku. Nkuku inakalipa.

2

Anagwilizana kuti wina amenyela bola mu goli ndipo wina agwile bola. Nkuku inangenesako kamozi. Ndipo inafika ntawi yakuti Bogololo amenyele bola mu goli.

3

Bongololo anamenya ndipo anagolesa. Bongololo anazugulusa bola ndipo anagolisa. Bongololo anamenya bola na mutu ndipo anagolesa. Bongololo anagolesa tusanu.

4

Nkuka inakalipa cifukwa inaluza. Nkuku inalikuluza kwambili. Bongololo anayamba kuseka naku kalipisa munzake.

5

Nkuku inakalipa kwambili ndipo inasegula kamwa namela Bongololo.

6

Pamene Nkuku inali kuyenda kunyumba inakumana na amake Bongololo. Amake Bongololo anafunsa nati, "Sunaoneko mwana wanga?" Nkuku siyinayanke. Amake Bongololo anada nkawa.

7

Amake Bongololo anamvela ka lizu kang'ono kapempa tandizo kwa amai ake. Amake Bongololo analanganisisa konse konse, ndipo anamvesesa. Lizu linali kumvekela mukati mwa Nkuku.

8

Amake Bongololo anakuwa nati, "Sewenzesa mpamvu zako zapadela mwana wanga!" Mabongololo yanunka kwambili ndipo siyamveka bwino mukamwa. Pamenepo, Nkuku inayamba kumvela kudwala.

9

Nkuku, inageya ndipo inavulula. Ndipo ina tunya nakumela. Ina etyemula naku kosomola.

10

Nkuku inakosomola mpaka inaluka Bongololo anali mumala, wamene inamela. Amake Bongololo na mwana wao anakwela mutengo ndipo anabisama.

11

Kucokela apo, pakati pa Nkuku na Bongololo pali cizondo.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nkuku na Bongololo
Author - Winny Asara
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Magriet Brink
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs